December 31–January 6
MACHITIDWE 19-20
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mukhale Tcheru ndi Kuyang’anira Gulu Lonse la Nkhosa”: (10 min.)
Mac. 20:28—Akulu ndi amene amaweta nkhosa mumpingo (w11 6/15 20-21 ¶5)
Mac. 20:31—Akulu amapereka thandizo “usana ndi usiku” ngati pakufunikira kutero (w13 1/15 31 ¶15)
Mac. 20:35—Akulu ayenera kukhala odzipereka kwambiri (bt 172 ¶20)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mac. 19:9—Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani yochita khama komanso kusintha ulaliki mogwirizana ndi anthu amene wawapeza? (bt 161 ¶11)
Mac. 19:19—Kodi anthu a ku Efeso anasonyeza chitsanzo chabwino chiti chomwe ifenso tiyenera kutengera? (bt 162-163 ¶15)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 19:1-20
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. M’patseni mwininyumbayo khadi lodziwitsa anthu za webusaiti yathu.
Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba lililonse komanso funso limene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) jl mutu 15
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muziphunzitsa Achinyamata Amene Akufuna Kuchita Zambiri Potumikira Yehova: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi akulu amagwira ntchito yofunika iti mumpingo? (Mac. 20:28) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kupitirizabe kuphunzitsa ena? Kodi akulu angatengere bwanji chitsanzo cha Yesu pa nkhani ya mmene ankaphunzitsira atumwi ake? Kodi abale amene akuphunzitsidwa ayenera kukhala ndi mtima wotani? (Mac. 20:35; 1 Tim. 3:1) Kodi akulu angaphunzitse ena zinthu ngati ziti? Kodi akulu ayenera kuwaona bwanji amene akuwaphunzitsa?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 19 ¶10-16 ndi bokosi lakuti “Kodi Asamariya Anachokera Kuti?”
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 60 ndi Pemphero