December 16-22
CHIVUMBULUTSO 13-16
Nyimbo Na. 55 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musamaope Zilombo Zoopsa”: (10 min.)
Chiv. 13:1, 2—Njoka inapereka mphamvu kwa chilombo chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10 (w12 6/15 8 ¶6)
Chiv. 13:11, 15—Chilombo cha nyanga ziwiri chinapereka moyo kwa chifaniziro cha chilombo choyamba chija (re 194 ¶26; 195 ¶30-31)
Chiv. 13:16, 17—Musalole kulandira chidindo cha chilombo (w09 2/15 4 ¶2)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Chiv. 16:13, 14—Kodi mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa bwanji “kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse”? (w09 2/15 4 ¶5)
Chiv. 16:21—Kodi ndi uthenga uti umene tidzalengeze dziko la Satanali lisanawonongedwe? (w15 7/15 16 ¶9)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Chiv. 16:1-16 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. (th phunziro 2)
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 5 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? kenako kambiranani naye mfundo za m’vidiyoyi. (th phunziro 11)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzisonyeza Kuti Simuli Mbali ya Dziko: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Zimene Timaganiza Komanso Kuchita Zizisonyeza Kuti Sitili Mbali ya Dziko. Kenako funsani omvera funso lakuti, Kodi mungatani kuti musakhale mbali ya dziko pa nkhani zokhudza maufulu a anthu komanso mmene boma likuyendetsera zinthu? Kenako oneraninso vidiyo yakuti Tisamachite Zinthu Zosonyeza Kuti Tili Mbali ya Dziko Tikakhala Pagulu. Kenako funsani omvera funso lakuti, Kodi mungakonzekere bwanji kuti musagonje ngati mutayesedwa kuti muchite zinthu zosonyeza kuti muli mbali ya dziko?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 64
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 130 ndi Pemphero