Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzisintha Ulaliki Wanu

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzisintha Ulaliki Wanu

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Odzozedwa ndi a nkhosa zina akuitanira anthu a mitundu yonse kuti ‘adzamwe madzi a moyo kwaulere.’ (Chiv. 22:17) Madzi ophiphiritsirawa akuimira zinthu zonse zomwe Yehova amapereka zothandiza anthu omvera kuti apulumuke ku uchimo ndi imfa. Choncho kuti tithandize anthu a zikhalidwe komanso zikhulupiriro zosiyanasiyana, tiyenera kuuza munthu aliyense “uthenga wabwino wosatha” m’njira yoti umufike pamtima.​—Chiv. 14:6.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muzisankha nkhani komanso lemba limene lingafike pamtima anthu a m’gawo lanu. Mungasankhe kugwiritsa ntchito chitsanzo chaulaliki kapena chitsanzo chilichonse chomwe chinakhala ndi zotsatira zabwino mutachigwiritsa ntchito. Kodi ndi nkhani ziti zomwe anthu amazikonda, nanga mungagwiritse ntchito malemba ati? Kodi ndi nkhani iti yomwe ili m’kamwam’kamwa panopo? Kodi ndi nkhani ziti zimene zingafike pamtima amuna kapena akazi?

  • Mungayambe ndi kupereka moni komanso kuchita zinthu zina zogwirizana ndi chikhalidwe cha anthu a m’dera lanu.2 Akor. 6:3, 4

  • Muzidziwa bwino mabuku, mavidiyo komanso zinthu zilizonse zomwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa, kuti muzigwiritse bwino ntchito pothandiza anthu achidwi

  • Mungapange dawunilodi zinthu zina zomwe zingakuthandizeni pokambirana ndi anthu a zinenero zosiyanasiyana omwe ali m’gawo lanu

  • Muzisintha uthenga wanu kuti ugwirizane ndi mwininyumba. (1 Akor. 9:19-23) Mwachitsanzo, kodi mungakambirane zotani ndi munthu amene waferedwa chaposachedwapa?

ONERANI VIDIYO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi nkhani yotani imene wofalitsa wayamba kukambirana ndi mwininyumba?

  • Kodi mwininyumbayu wakhala akukumana ndi mavuto otani?

  • Kodi ndi malemba ati amene akanakhala oyenera pa nthawiyi, ndipo n’chifukwa chiyani?

  • Kodi inuyo mumasintha bwanji ulaliki wanu kuti uwafike pamtima anthu a m’gawo lanu?