Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Dziko “Linameza Mtsinje”

Dziko “Linameza Mtsinje”

Kuyambira kale, olamulira a dziko akhala akuthandiza anthu a Yehova. (Ezara 6:1-12; Esitere 8:10-13) Ngakhale masiku ano “dziko,” lomwe likuimira anthu a maganizo oyenera omwe ali ndi mphamvu m’dzikoli, limameza “mtsinje” wamavuto amene “njoka,” yomwe ndi Satana Mdyerekezi, amabweretsera atumiki a Yehova. (Chiv. 12:16) Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amatipulumutsa,” amatha kugwiritsa ntchito olamulira a dzikoli kuti athandize anthu ake.​—Sal. 68:20; Miy. 21:1.

Nanga bwanji ngati munamangidwa chifukwa cha zimene mumakhulupirira? Musakayikire kuti Yehova akuona zimene zikukuchitikirani. (Gen. 39:21-23; Sal. 105:17-20) Musamakayikirenso kuti Yehova adzakudalitsani kwambiri komanso musamaiwale kuti kukhulupirika kwanu kumalimbikitsa abale ndi alongo padziko lonse.​—Afil. 1:12-14; Chiv. 2:10.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ABALE A KU KOREA ATULUTSIDWA M’NDENDE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani abale ambiri a ku South Korea ankamangidwa?

  • Kodi khoti linagamula zotani kuti abale athu atulutsidwe m’ndende?

  • Kodi tingathandize bwanji abale athu padziko lonse omwe ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo?

  • Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito bwanji ufulu umene tili nawo panopa?

  • Kodi ndi ndani amene amatithandiza kuti tipambane milandu yosiyanasiyana?

Kodi ndimagwiritsa ntchito bwanji ufulu umene ndili nawo panopa?