Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 10-12

“Mboni Ziwiri” Zinaphedwa Koma Zinakhalanso ndi Moyo

“Mboni Ziwiri” Zinaphedwa Koma Zinakhalanso ndi Moyo

11:3-11

  • “Mboni ziwiri”: Gulu laling’ono la abale odzozedwa omwe ankatsogolera pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914

  • Zinaphedwa: Zitalalikira kwa zaka zitatu ndi hafu “zitavala ziguduli,” tinganene kuti mbonizi “zinaphedwa” pamene zinaikidwa m’ndende n’kusiya kugwira ntchito yawo

  • Zinakhalanso ndi moyo: Masiku atatu ndi hafu ophiphiritsawa atatha, mbonizi zinakhalanso ndi moyo pamene zinatuluka m’ndende n’kukapitiriza kutsogolera ntchito yolalikira