MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mungakonde Kufunsira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?
Kodi muli ndi zaka zoyambira 23 mpaka 65 ndipo mukuchita utumiki wa nthawi zonse? Kodi ndinu wathanzi komanso mutha kukatumikira kulikonse kumene kukufunika ofalitsa ambiri? Ngati mwayankha kuti inde pa mafunsowa, kodi munaganizirapo zolowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? Kungochokera pamene sukuluyi inayamba, mabanja, abale osakwatira komanso alongo osakwatiwa ambirimbiri afunsira kuti akalowe sukuluyi. Koma tikufuna kuti abale ambiri osakwatira afunsire sukulu imeneyi. Mupemphe Yehova kuti akupatseni mtima wofunitsitsa kumusangalatsa komanso kutsanzira Mwana wake. (Sl 40:8; Mt 20:28; Ahe 10:7) Kenako mungachite bwino kuganizira mmene mungachepetsere ntchito kapena maudindo amene muli nawo kuti muyenerere kupita kusukuluyi.
Kodi anthu amene amaliza sukulu imeneyi akhala ndi mwayi wotumikira m’njira ziti? Ena apatsidwa mwayi wokatumikira kudera limene amalankhula chilankhulo china, pomwe ena apatsidwa utumiki wapadera wolalikira m’malo opezeka anthu ambiri m’mizinda. Enanso amakhala oyang’anira madera ogwirizira, oyang’anira madera kapena amishonale. Mukamaganizira zinthu zimene mungachite potumikira Yehova, yesetsani kukhala ndi mtima wa mneneri Yesaya yemwe anati: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”—Yes 6:8.
ONERANI VIDIYO YAKUTI AMISHONALE AMAGWIRA NTCHITO YOKOLOLA, KENAKO FUNSANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi amishonale amasankhidwa bwanji?
-
Kodi amishonale akugwira ntchito yotani?
-
Kodi ndi madalitso otani amene amishonale amapeza?