MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Timasonyeza Chikondi Tikamachita Zinthu Mogwirizana Ndi Chilango Chochokera kwa Yehova
Kuchotsa munthu mumpingo kumateteza mpingowo komanso kumathandiza munthu wosalapayo. (1Ak 5:6, 11) Tikamachita zinthu mogwirizana ndi chilango chochokera kwa Yehova choterechi, timasonyeza chikondi. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo imeneyi ndi yoona ngakhale kuti chilangochi chimakhala chopweteka kwa onse okhudzidwa, kuphatikizapo achibale a munthuyo komanso a m’komiti yoweruza mlandu?
Chofunika kwambiri n’chakuti timasonyeza kuti timakonda Yehova. Zili choncho chifukwa choti timasonyeza kuti timafuna kuyeretsa dzina lake komanso timaona kuti mfundo zake n’zoyera. (1Pe 1:14-16) Timasonyezanso kuti timakonda munthu amene wachotsedwayo. Chilango chokhwima chimapweteka koma chingabale “chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.” (Ahe 12:5, 6, 11) Koma timasokoneza chilango cha Yehova ngati timachezabe ndi munthu amene wachotsedwa kapena wadzilekanitsa ndi mpingo. Tisaiwale kuti Yehova amalanga anthu ake “pa mlingo woyenera.” (Yer 30:11) Choncho tikamachita zinthu mogwirizana ndi chilango cha Yehova komanso kuchitabe zinthu zokhudza kulambira, timayembekezera kuti tsiku lina munthuyo adzabwerera kwa Atate wathu wachifundo.—Yes 1:16-18; 55:7.
-
Kodi makolo a Chikhristu zimawapweteka bwanji mwana wawo akasiya Yehova?
-
Kodi anthu mumpingo angathandize bwanji achibale okhulupirika?
-
Kodi ndi nkhani iti ya m’Baibulo imene imasonyeza kuti kukhala okhulupirika kwa Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kukhala okhulupirika kwa achibale athu?
-
Kodi timasonyeza bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa achibale athu?