Tizikonda Yehova Kuposa Mmene Timakondera Achibale Athu
Wachibale wathu akachotsedwa zingakhale zovuta kusonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova. Akhristu omwe achibale awo ndi ochotsedwa angaphunzire mfundo yofunika pa malangizo amene Yehova anapatsa Aroni. Tiyenera kukonda kwambiri Yehova kuposa mmene timakondera achibale athu osakhulupirika.
Kodi Akhristu amene amachita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehova okhudza anthu ochotsedwa amapeza madalitso otani?—1Ak 5:11; 2Yo 10, 11