Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Itanirani Anthu Onse M’gawo Lanu ku Chikumbutso!

Itanirani Anthu Onse M’gawo Lanu ku Chikumbutso!

Ntchito yapadera yoitanira anthu ku Chikumbutso iyamba pa February 27. Tikufunitsitsa kuitanira anthu ambiri kumwambo wokumbukira imfa ya Khristu umenewu. Komanso tiyenera kuonetsetsa anthu amene asonyeza chidwi n’kuwathandiza.

ZIMENE MUNGACHITE

PEREKANI KAPEPALA

“Tikupereka kapepala aka kwa anthu powaitanira kumwambo wofunika kwambiri. Pa March 23, anthu ambiri padziko lonse adzasonkhana kuti akumbukire imfa ya Yesu Khristu. Pamwambowo adzamvetsera nkhani yofotokoza mmene imfa ya Yesu imatithandizira. Zonsezi zidzachitika popanda kuyendetsa mbale ya zopereka. Malo komanso nthawi imene mwambowu udzachitike, talemba papepalali. Muyesetse kudzabwera.”

Ngati munthuyo wasonyeza chidwi chitani izi:

  • PEREKANI NSANJA YA OLONDA

    Muuzeni nkhani imene mudzakambirane ulendo wotsatira.

  • ONETSANI VIDIYO YA CHIKUMBUTSO

    Muuzeni zimene mudzaphunzire ulendo wotsatira.

Mukadzakumananso mukhoza kudzachita zotsatirazi:

  • ONETSANI VIDIYO YAKUTI N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPHUNZIRA BAIBULO?

    Kenako perekani buku kapena kabuku koti muziphunzira naye.

  • PEREKANI BUKU LAKUTI KODI BAIBULO LIMAPHUNZITSA CHIYANI KWENIKWENI?

    Kambiranani mfundo zokhudza Chikumbutso patsamba 206-208. Kenako perekani bukulo.

  • PEREKANI KABUKU KAKUTI MVERANI MULUNGU

    Kambiranani tsamba 18-19 kuti aone mmene imfa ya Khristu imatithandizira.