MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu
Chiyembekezo chili ngati nangula amene amathandiza kuti sitima isasunthe. (Aheb. 6:19) Zili choncho chifukwa chimatithandiza kuti tisasokonezeke mwauzimu tikakumana ndi mavuto aakulu okhala ngati mafunde oopsa. (1 Tim. 1:18, 19) Mavutowa akhoza kukhala matenda aakulu, mavuto azachuma, imfa ya munthu amene tinkamukonda kapena mayesero ena alionse.
Chikhulupiriro komanso chiyembekezo chimatithandiza kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono zimene Mulungu watilonjeza. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 11:13, 26, 27) Choncho kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tiyenera kumaganizira kwambiri zimene Mulungu walonjeza m’Mawu ake. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhalabe osangalala pamene takumana ndi mayesero.
ONERANI VIDIYO YAKUTI TIZISANGALALA NDI CHIYEMBEKEZO CHATHU. KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
N’chifukwa chiyani Mose ndi chitsanzo chabwino?
-
Kodi amuna okwatira ali ndi udindo wotani m’banja?
-
Kodi ndi nkhani ziti zimene mungakambirane pa Kulambira kwa Pabanja?
-
Kodi kukhala ndi chiyembekezo kungakuthandizeni bwanji kuti musataye mtima mukakumana ndi mayesero?
-
Kodi inuyo mukuyembekezera zinthu ziti?