Akuphunzitsa choonadi ku Cambodia

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU February 2018

Zimene Tinganene

Kukambirana pogwiritsa ntchito mafunso otsatirawa: Kodi inuyo mumaona kuti Baibulo ndi lothandizabe masiku ano? Kodi zimene Baibulo limanena zimagwirizana ndi sayansi? Kodi malangizo a m’Baibulo ndi othandizadi?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Fanizo la Tirigu ndi Namsongole

Kodi Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la tirigu ndi namsongole pofuna kunena za chiyani? Kodi ndi ndani yemwe ali wofesa mbewu, mdani, komanso okolola?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mfundo Zimene Tingaphunzire Kuchokera M’mafanizo Onena za Ufumu

Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo osavuta kumva pophunzitsa mfundo zozama zachoonadi. Kodi tingaphunzire chiyani pa Mateyu 13?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesu Amadyetsa Anthu Ambiri Kudzera Mwa Anthu Ochepa

Yesu anauza ophunzira ake kuti adyetse khamu la anthu ngakhale kuti anali ndi mikate 5 komanso nsomba ziwiri zokha. Kodi chinachitika n’chiyani, nanga zimenezi zinkatanthauza chiyani?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”

Pamene Yesu anali padzikoli, anauza anthu lamulo lakuti: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” Kodi tiyenera kumvera lamuloli ngakhale makolo athu atakalamba?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Mumayendera Maganizo a Ndani?

Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizitsogoleredwa ndi Mulungu osati Satana? Yesu anatchula zinthu zitatu zomwe zingatithandize kuti tisamakhale ndi maganizo olakwika.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki​—Muzigwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso

Yesu ankakonda kufunsa mafunso amene ankachititsa ophunzira ake kufotokoza maganizo awo. Kodi tingatengere bwanji chitsanzo chake tikamalalikira komanso kuphunzitsa anthu?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Tizipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakhumudwitse Ena

Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa anthu za kuopsa kochita zinthu zimene zingatipunthwitse komanso kukhumudwitsa ena. Kodi n’chiyani pa moyo wanu chimene chingakhale chopunthwitsa?