Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

February 26–​March 4

MATEYU 18-19

February 26–​March 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • Tizipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakhumudwitse Ena”: (10 min.)

    • Mat. 18:6, 7​—Tiziyesetsa kuti tisamakhumudwitse ena (”chimwala cha mphero . . . ngati chimene bulu amayendetsa” zopunthwitsa” Mwala wamphero” ”Mwala Wamphero Wapamwamba ndi Wapansi” zithunzi ndi mavidiyo,mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:6, 7, nwtsty)

    • Mat. 18:8, 9​—Tizipewa chilichonse chimene chingatipunthwitse (“Gehena” mfundo zimene ndikuphunzira komanso matanthauzo a mawu ena pa Mat. 18:8, 9, nwtsty)

    • Mat. 18:10​—Yehova amadziwa tikachita zinthu zokhumudwitsa ena (amaona nkhope ya Atate wanga“ mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:10, nwtsty; w10 11/1 16)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • Mat. 18:21, 22​—Kodi tiyenera kukhululukira m’bale wathu kangati? (”nthawi 77” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:22, nwtsty)

    • Mat 19:7​—Kodi “kalata yothetsa ukwati” inkagwira ntchito yotani? (“kalata yothetsa ukwati” mfundo zimene ndikuphunzira komanso zithunzi ndi mavidiyo pa Mat 19:7, nwtsty)

    • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 18:18-35

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene.

  • Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba lililonse ndipo gawirani buku kapena kabuku kamene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu.

  • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 26 ¶18-20—Sonyezani mmene tingafikire pamtima wophunzira.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 90

  • Pewani Kuchita Chilichonse Chomwe Chingakhumudwitse Ena (2 Akor. 6:3): (9 min.) Onetsani vidiyoyi.

  • Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa 3 March: (6 min.) Nkhani yochokera mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya February 2016, Itanirani Anthu Onse M’gawo Lanu ku Chikumbutso”. Perekani kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kwa aliyense n’kukambirana mfundo zake. Fotokozani kuti nkhani yapadera idzakhala ndi mutu wakuti “Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani Kwenikweni?” ndipo idzakambidwa mlungu wa March 19, 2018. Nkhaniyi idzathandiza anthu kuyembekezera mwachidwi mwambo wa Chikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wakonza pofuna kuti mudzathe kugawira timapepalati kwa anthu onse a m’gawo lanu.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 14 ¶15-23 komanso bokosi patsamba 156

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 133 ndi Pemphero