Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 18-19

Tizipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakhumudwitse Ena

Tizipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakhumudwitse Ena

Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa anthu za kuopsa kochita zinthu zimene zingatipunthwitse komanso kukhumudwitsa ena.

18:6, 7

  • Mawu akuti “zopunthwitsa” akutanthauza zochita kapena zinthu zina zimene zingachititse munthu kuti achite zinthu zolakwika, kapenanso achite tchimo

  • Munthu wokhumudwitsa ena zikanakhala bwino kumuponya m’nyanja atamangiriridwa chimwala cha mphero m’khosi mwake

Mwala wa mphero

18:8, 9

  • Yesu anauza otsatira ake kuti ayenera kuchotsa ngakhale chiwalo chawo chofunika kwambiri monga dzanja kapena diso ngati akuona kuti chiwalocho chikuwachititsa kuti achite tchimo

  • Kuli bwino kukhala wopanda chinthu chinachake chimene timachikonda kwambiri n’kudzalowa mu Ufumu wa Mulungu kusiyana ndi kukhala ndi chinthucho koma n’kudzaponyedwa m’Gehena, yemwe akutanthauza kuwonongedwa kotheratu

Kodi n’chiyani pa moyo wanga chimene chingakhale chopunthwitsa, nanga ndingatani kuti ndizipewa zinthu zimene zingandipunthwitse komanso kukhumudwitsa ena?