Yesu Amadyetsa Anthu Ambiri Kudzera Mwa Anthu Ochepa
Pasika wa mu 32 C.E. atayandikira, Yesu anachita chozizwitsa chimene chinalembedwa ndi anthu onse 4, omwe analemba mabuku a Uthenga Wabwino.
Yesu anakhazikitsa njira imene akuigwiritsabe ntchito masiku ano, yomwe ndi yofanana ndi zimene anachita pa nthawi ya chozizwitsachi.
-
Yesu anauza ophunzira ake kuti adyetse khamu la anthu ngakhale kuti anali ndi mikate 5 komanso nsomba ziwiri zokha
-
Yesu anatenga mitanda ya mkate ndi nsomba zija ndipo atapemphera, anapatsa ophunzira ake omwe anagawira khamu la anthulo
-
Mozizwitsa, chakudyacho chinakwanira moti anthu onse anadya n’kukhuta. Yesu anadyetsa anthu ambiri kudzera mwa ophunzira ake omwe anali ochepa
-
Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza adzakhazikitsa njira yoperekera “chakudya pa nthawi yoyenera.”—Mat. 24:45
-
Mu 1919, Yesu anasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” yemwe ndi kagulu ka Akhristu odzozedwa, kuti aziyang’anira “antchito ake apakhomo” omwe ndi anthu odyetsedwa
-
Pogwiritsa ntchito kagulu ka Akhristu odzozedwawa, Yesu akutsatira njira yofanana ndi imene anagwiritsa ntchito m’nthawi ya atumwi
Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimazindikira komanso kulemekeza njira imene Yesu akugwiritsa ntchito podyetsa anthu?