Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”

“Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”

Pamene Yesu anali padzikoli, anauza anthu lamulo lakuti: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Eks. 20:12; Mat. 15:4) Yesu anali ndi ufulu wolankhula pa nkhaniyi chifukwa iye ali mwana ‘anapitiriza kumvera’ makolo ake. (Luka 2:51) Atakula, anakonza zoti mayi ake asamaliridwe bwino iyeyo akamwalira.​—Yoh. 19:26, 27.

Masiku anonso, achinyamata achikhristu omwe amamvera makolo awo komanso kulankhula nawo mwaulemu, amasonyeza kuti amawalemekeza. Lamulo loti tizilemekeza makolo athu limagwirabe ntchito ngakhale makolowo atakalamba. Tingasonyeze kuti timawalemekezabe tikamafunsira nzeru kwa iwo. (Miy. 23:22) Timalemekezanso makolo athu okalamba tikamawasamalira ndi kuwapatsa zofunika pa moyo wawo ngati pakufunika kutero. (1 Tim. 5:8) Kaya ndife achichepere kapena achikulire, kuyesetsa kulankhulana ndi makolo athu kungatithandize kuti tiziwalemekeza.

ONERANI VIDIYO YAKUTI KODI NDINGATANI KUTI NDIZILANKHULANA BWINO NDI MAKOLO ANGA? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani nthawi zina zingakhale zovuta kulankhulana ndi makolo anu?

  • Kodi mungalemekeze bwanji makolo anu mukamalankhula nawo?

  • N’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kuti muzilankhula ndi makolo anu? (Miy. 15:22)

Kulankhulana ndi makolo anu kungathandize kuti zinthu zizikuyenderani bwino