Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 12-13

Fanizo la Tirigu ndi Namsongole

Fanizo la Tirigu ndi Namsongole

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la tirigu ndi namsongole posonyeza nthawi komanso zimene adzachite akamadzasankha Akhristu odzozedwa omwe ali ngati tirigu, zomwe zinayamba kuchitika mu 33 C.E.

13:24

‘Munthu anafesa mbewu zabwino m’munda wake’

  • Wofesa mbewu: Yesu Khristu

  • Mbewu zabwino zinafesedwa: Ophunzira a Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera

  • Munda: Anthu

13:25

“Anthu ali m’tulo, kunabwera mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole m’munda wa tiriguwo”

  • Mdani: Mdyerekezi

  • Anthu ali m’tulo: Atumwi onse atamwalira

13:30

“Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola”

  • Tirigu: Akhristu odzozedwa

  • Namsongole: Akhristu onyenga

“Choyamba sonkhanitsani namsongole . . .  Mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu”

  • Akapolo kapena okolola: Angelo

  • Kusonkhanitsa namsongole: Akhristu onyenga akusiyanitsidwa ndi Akhristu odzozedwa

  • Kusonkhanitsa tirigu n’kukamuika munkhokwe: Akhristu odzozedwa akusonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu

Pamene ntchito yokolola inkayamba, kodi n’chiyani chinasiyanitsa Akhristu oona ndi onyenga?

Kodi ndingapindule bwanji ngati nditamvetsa tanthauzo la fanizoli?