Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Pitirizani Kudikira Mopirira

Pitirizani Kudikira Mopirira

Kodi mwakhala mukudikira kwa nthawi yaitali bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ubwere? Kodi mukupitirizabe kudikira mopirira ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto? (Aroma 8:25) Akhristu ena amatsutsidwa, kuzunzidwa, kutsekeredwa m’ndende ngakhale kufuna kuphedwa kumene. Enanso akupirira mayesero monga matenda aakulu komanso ukalamba.

Kodi n’chiyani chingatithandize kupitiriza kudikira mopirira ngakhale tikukumana ndi mavuto amenewa? Tingalimbitse chikhulupiriro chathu tikamawerenga Baibulo komanso kusinkhasinkha zimene tawerengazo. Tiziganizira kwambiri zimene tikuyembekezera m’tsogolomu. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 12:2) Komanso tizipempha mochonderera kwa Yehova kuti atipatse mphamvu yake ya mzimu woyera. (Luka 11:10, 13; Aheb. 5:7) Yehova yemwe ndi Atate wathu wachikondi angatithandize “kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.”​—Akol. 1:11.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, TIYENERA ‘KUTHAMANGA MOPIRIRA’​—MUSAMAKAYIKIRE KUTI MUDZAPEZA MPHOTO NDIPO KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi “zinthu zosayembekezereka” ziti zimene zingachitike pa moyo wathu? (Mlal. 9:11)

  • Kodi pemphero lingatithandize bwanji tikamakumana ndi mayesero?

  • Ngati panopa sitingathenso kutumikira Yehova ngati kale, n’chifukwa chiyani tiyenera kumangochita zimene tingakwanitse?

  • Muziyang’anabe pamphoto

    N’chiyani chimene chimakuthandizani kuti musamakayikire kuti mudzalandira mphoto?