Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 9-11

Fanizo la Mtengo wa Maolivi

Fanizo la Mtengo wa Maolivi

11:16-26

Kodi mbali zosiyanasiyana za mtengo wa maolivi wotchulidwa m’mavesiwa zimaimira chiyani?

  • Mtengo: kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu chokhudza pangano la Abulahamu

  • Thunthu: Yesu, yemwe ndi mbali yoyambirira ya mbewu ya Abulahamu

  • Nthambi: chiwerengero chokwanira cha mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu

  • Nthambi zomwe “zinadulidwa”: mtundu wa Isiraeli womwe unakana Yesu

  • Nthambi zomwe ‘zinalumikizidwa’: Akhristu odzozedwa ochokera m’mitundu yonse

Monga mmene ulosi umanenera, mbewu ya Abulahamu yomwe ndi Yesu komanso Akhristu odzozedwa okwana 144,000, idzabweretsa madalitso “kwa anthu a mitundu ina.”​—Aroma 11:12; Gen. 22:18

Kodi ndikuphunzira zotani zokhudza Yehova pa nkhani ya mmene anakwaniritsira cholinga chake chonena za mbewu ya Abulahamu?