Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumaona Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso?

Kodi Mumaona Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso?

Kodi mumachita chidwi mukamaona zimene Mulungu analenga monga maluwa okongola, nyenyezi kapenanso mathithi ochititsa chidwi? Zinthu za m’chilengedwe zimatithandiza kuona makhalidwe a Yehova osaoneka ndi maso. (Aroma 1:20) Tikamaganizira zimene timaona m’chilengedwe, timatha kuzindikira kuti Mulungu ali ndi makhalidwe monga mphamvu, chikondi, nzeru, chilungamo komanso kuwolowa manja.​—Sal. 104:24.

Kodi ndi zinthu zina ziti zimene Mulungu analenga zomwe mumaona tsiku lililonse? Ngakhale zitakhala kuti mumakhala m’tawuni, mukhozabe kuona zinthu monga mbalame kapena mitengo. Kuchita chidwi ndi zimene Yehova analenga kungatithandize kuti tichepetse nkhawa, tiziona mavuto athu moyenera komanso kuti tizikhulupirira kwambiri kuti iye ali ndi mphamvu zotha kutisamalira mpaka kalekale. (Mat. 6:25-32) Ngati muli ndi ana mungachite bwino kuwathandiza kuti azichita chidwi ndi chilengedwe kuti aone makhalidwe abwino a Mulungu. Tikamayamikira zinthu zimene zili m’chilengedwe timayandikira Mlengi wathu.​—Sal. 8:3, 4.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZACHILENGEDWE ZIMATIPHUNZITSA ZA ULEMERERO WA MULUNGU​—KUWALA KOMANSO MITUNDU YA ZINTHU, KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi n’chiyani chimatithandiza kuti tiziona mitundu ya zinthu?

  • N’chiyani chimachititsa kuti zinthu zizioneka monyezimira komanso ngati zikusintha mtundu?

  • N’chifukwa chiyani timaona mitundu yosiyanasiyana m’mlengalenga?

  • Ndi mitundu yochititsa chidwi iti ya zinthu zimene Mulungu analenga yomwe mumaona mukakhala kunyumba kwanu?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumachita chidwi ndi zinthu zachilengedwe?

Kodi kuwala komanso mitundu ya zinthu zimatithandiza bwanji kudziwa makhalidwe a Yehova?