January 25-31
EZARA 6-10
Nyimbo Na. 10 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Amafuna Kuti Tizimutumikira ndi Mtima Wonse”: (10 min.)
Ezara 7:10—Ezara anakonzekeretsa mtima wake
Ezara 7:12-28—Ezara anakonzekera kubwerera ku Yerusalemu
Ezara 8:21-23—Ezara ankakhulupirira kuti Yehova ateteza atumiki ake
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Ezara 9:1, 2—N’chifukwa chiyani kukwatirana ndi anthu a mitundu ina kunali koopsa? (w06 1/15 20 ndime 1)
Ezara 10:3—N’chifukwa chiyani ana anachotsedwa pamodzi ndi akazi? (w06 1/15 20 ndime 2)
Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: Ezara 7:18-28 (Osapitirira 4 min.)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gawirani kabuku kakuti Uthenga Wabwino, kenako kambiranani phunziro 8, funso 1 ndime 1. Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza ulendo wobwereza kwa munthu amene analandira kabuku kakuti Uthenga Wabwino. Mukambirane naye phunziro 8, funso 1 ndime 2. Mumuuze nkhani imene mudzaphunzire ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) Chitani chitsanzo cha munthu akuchititsa phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino phunziro 8, funso 2.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki: Muzisiya Mafunso Oti Mudzakambirane Ulendo Wotsatira”: (7 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo ya mutu wakuti Luso Loti Tiwonjezere mu January. Vidiyoyi ikusonyeza ofalitsa akufunsa mwininyumba funso lomwe lingamuthandize kuti adzachite ulendo wobwereza atagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a mwezi wa January komanso kabuku ka Uthenga Wabwino.
Zofunika pampingo: (8 min.)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 25 ndime 1-8, (30 min.)
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu wa Mawa (3 min.)
Nyimbo Na. 120 ndi Pemphero