January 30–February 5
YESAYA 43-46
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Ndi Mulungu Yemwe Amalosera Zoona”: (10 min.)
Yes. 44:26-28—Yehova analosera kuti Yerusalemu ndiponso kachisi adzamangidwanso komanso kuti Koresi ndi amene adzagonjetse Babulo (ip-2 71-72 ¶22-23)
Yes. 45:1, 2—Yehova ananeneratu mmene Babulo adzagonjetsedwere (ip-2 77-78 ¶4-6)
Yes. 45:3-6—Yehova anafotokoza chifukwa chake anagwiritsa ntchito Koresi kuti agonjetse Babulo (ip-2 79-80 ¶8-10)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yes. 43:10-12—Kodi Aisiraeli anayenera kuchita chiyani kuti akhale mboni za Yehova? (w14 11/15 21-22 ¶14-16)
Yes. 43:25—Kodi chifukwa chachikulu chimene Yehova amafafanizira zolakwa zathu n’chiyani? (ip-2 60 ¶24)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yes. 46:1-13
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) kt—Kulalikira mnzanu wakusukulu kapena wakuntchito.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) kt—Siyani funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) jl mutu 4
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?: (15 min.) Onetsani vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? Kenako kambiranani mafunso awa: Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vidiyoyi tikamalalikira mwamwayi, pamalo opezeka anthu ambiri komanso kunyumba ndi nyumba? Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zimene mwakumana nazo pogwiritsa ntchito vidiyoyi?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 16 ¶16-29, bokosi patsamba 142 komanso Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 144.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero