January 1-7
MATEYU 1-3
Nyimbo Na. 14 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ufumu Wakumwamba Wayandikira”: (10 Min.)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mateyu.]
Mat. 3:1, 2—Yohane M’batizi ankalalikira kuti Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kufika (“kulalikira” “ufumu” “ufumu wakumwamba” “wayandikira” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 3:1, 2, nwtsty)
Mat. 3:4—Yohane M’batizi ankakhala moyo wosalira zambiri ndipo ankadzipereka ndi mtima wonse pochita chifuniro cha Mulungu (“Zovala za Yohane M’batizi Komanso Maonekedwe Ake” “Dzombe” “Uchi” zithunzi ndi mavidiyo za pa Mat. 3:4, nwtsty)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mat. 1:3—N’chifukwa chiyani Mateyu pofotokoza mzere womwe Yesu anabadwira anaphatikizapo mayina a azimayi 5? (“Tamara” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 1:3, nwtsty)
Mat. 3:11—Kodi tikudziwa bwanji kuti munthu amene akubatizidwa ayenera kuviikidwa m’madzi? (“ndikukubatizani” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 3:11, nwtsty)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 1:1-17
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Onani chitsanzo cha ulaliki.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 41-42 ¶6-7
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Lipoti la Chaka Chautumiki: (15 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Pambuyo powerenga kalata yochokera ku ofesi ya nthambi yonena za lipoti la chaka chautumiki chapitachi, funsani ofalitsa omwe munawasankhiratu, omwe anakumana ndi zinthu zosangalatsa m’chakacho.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 12 ¶9-15, bokosi patsamba 122-123, komanso tsamba 130-131
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 137 ndi Pemphero