January 15-21
Mateyu 6-7
Nyimbo Na. 21 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba”: (10 min.)
Mat. 6:10—Yesu anatchula Ufumu wa Mulungu koyambirira m’pemphero lachitsanzo, zomwe zikusonyeza kuti ndi wofunika kwambiri (bhs 178 ¶12)
Mat. 6:24—N’zosatheka kumatumikira Mulungu ndi “chuma” nthawi imodzi (“Kapolo”mfundo zimene ndikuphunzira, pa Mat. 6:24, nwtsty)
Mat. 6:33—Yehova amapereka zinthu zofunikira kwa atumiki ake okhulupirika omwe amaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba (“pitirizani kufunafuna Ufumu” “chilungamo” ”chake” mfundo zimene ndikuphunzirapa Mat. 6:33, nwtsty; w16.07 12 ¶18)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mat. 7:12—Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vesili tikamakonzekera zoti tikalankhule mu utumiki? (w14 5/15 14-15 ¶14-16)
Mat. 7:28, 29—Kodi anthu anakhudzidwa bwanji ndi zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo n’chifukwa chiyani zinawakhudza choncho? (“linadabwa” kaphunzitsidwe kake “osati monga alembi awo” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 5:28, 29, nwtsty)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 6:1-18
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki. Munthu yemwe munacheza naye ulendo wapita simunamupeze pakhomo, ndiye mwakumana ndi wachibale wake.
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri (Osapitirira 5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Musamade Nkhawa”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuonetsa vidiyo yakuti Zimene Tikuphunzira pa Mafanizo Amene Yesu Ananena—Onetsetsani Mbalame ndi Maluwa.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 13 ¶1-10 komanso tsamba 132-133
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 132 ndi Pemphero