KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Musamade Nkhawa
Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anati: “Lekani kudera nkhawa moyo wanu.” (Mat. 6:25) Mwachibadwa, anthu ochimwafe timakonda kuda nkhawa. Kuwonjezera pamenepo, m’dziko la Satanali timakumana ndi zinthu zambiri zodetsa nkhawa. Komabe Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti ayenera kupewa kuda nkhawa kwambiri. (Sal. 13:2) Ananena zimenezi chifukwa ankadziwa kuti kudera nkhawa ngakhale pa zofunika zatsiku ndi tsiku, kungatisokoneze komanso kungapangitse kuti tizilephera kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. (Mat. 6:33) Pali mfundo zinanso zimene Yesu anatchula zomwe zingatithandize kuti tisamadere nkhawa zinthu zosafunika kwenikweni.
-
Mat. 6:26—Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera kwa mbalame? (w16.07 9-10 ¶11-13)
-
Mat. 6:27—N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuda nkhawa kumangowonongetsa nthawi komanso mphamvu? (w05 11/1 22 ¶5)
-
Mat. 6:28-30—Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera ku maluwa akutchire? (w16.07 10-11 ¶15-16)
-
Mat. 6:31, 32—Kodi Akhristu amasiyana bwanji ndi anthu ena? (w16.07 11 ¶17)
Kodi ndi zinthu ziti zimene ndikufuna ndisiye kuzidera nkhawa?