January 22-28
MATEYU 8-9
Nyimbo Na. 17 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yesu Ankakonda Anthu”: (10 min.)
Mat. 8:1-3—Yesu anachitira chifundo munthu wodwala khate (“kumukhudza” ”Ndikufuna” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 8:3, nwtsty)
Mat. 9:9-13—Yesu ankakonda anthu omwe ankanyozedwa ndi ena (“kudya patebulo” “okhometsa msonkho” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 9:10, nwtsty)
Mat. 9:35-38—Kukonda anthu kunachititsa kuti Yesu azilalikira uthenga wabwino ngakhale atatopa ndiponso anapempha Mulungu kuti atumize antchito ambiri oti agwire ntchitoyi (“anawamvera chisoni” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 9:36, nwtsty)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mat. 8:8-10—Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yesu anakambirana ndi mkulu wa asilikali? (w02 8/15 13 ¶16)
Mat. 9:16, 17—Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pofotokoza mafanizo awiriwa? (jy 70 ¶6)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 8:1-17
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene. Muitanireni ku misonkhano yathu.
Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba komanso buku limene mukufuna kugwiritsa ntchito.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 47 ¶18-19
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
‘Mulungu Anamuika Kukhala Ambuye ndi Khristu’—Mbali Yoyamba—Mbali ina ya vidiyoyi: (15 min.) Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 9:18-25, kenako onerani mbali ya vidiyoyi. Mukamaliza kambiranani mafunso otsatirawa:
Kodi Yesu anasonyeza bwanji chifundo kwa Yairo komanso mzimayi wina yemwe ankadwala?
Kodi nkhaniyi yakuthandizani bwanji kukhulupirira maulosi a m’Baibulo onena zimene zidzachitike Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira?
Kodi tingatsanzire Yesu pa nkhani yokonda anthu m’njira zina ziti?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 13 ¶11-23
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero