Yesu Ankakonda Anthu
Pa Mateyu 8 ndi 9 amafotokoza zokhudza utumiki wa Yesu ku Galileya. Pamene Yesu ankachiritsa anthu, anasonyeza kuti anali ndi mphamvu, koma chofunika kwambiri n’chakuti anasonyezanso kuti amakonda kwambiri anthu ndiponso kuti ndi wachifundo.
-
Yesu anachiritsa munthu wakhate.—Mat. 8:1-3
-
Yesu anachiritsa wantchito wa mkulu wa asilikali.—Mat. 8:5-13
Anachiritsa apongozi aakazi a Petulo.—Mat. 8:14, 15
Anatulutsa ziwanda ndiponso anachiritsa odwala.—Mat. 8:16, 17
-
Yesu anatulutsa ziwanda mwa amuna awiri ochititsa mantha ndipo anazitumiza kuti zikalowe m’gulu la nkhumba.—Mat. 8:28-32
-
Yesu anachiritsa munthu wakufa ziwalo.—Mat. 9:1-8
Anachiritsa mayi wina amene anagwira chovala chake ndiponso anaukitsa mwana wa Yairo.—Mat. 9:18-26
Anachiritsa munthu wosalankhula komanso akhungu.—Mat. 9:27-34
-
Yesu ankayenda m’mizinda ndi m’midzi kuchiritsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.—Mat. 9:35, 36
Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimakonda anthu ena?