MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Tingatsatire Bwanji Malangizo Akuti Ukayanjane Ndi M’bale Wako Choyamba?
Tayerekezerani kuti munkakhala ku Galileya m’nthawi ya Yesu. Tsiku lina mukunyamuka n’kupita ku Yerusalemu kuti mukakhale nawo pa Chikondwerero cha Misasa. Mumzindawu mwadzadza olambira anzanu amene achokera m’madera osiyanasiyana. Inuyo mukufuna kukapereka nsembe kwa Yehova ndipo mukukoka mbuzi yanu n’kudutsa movutikira m’chigulu cha anthu omwe ali mumzindawo n’kumalowera kukachisi. Mutafika kukachisiko, mwapeza kuti kuli anthu ambirimbiri omwe nawonso akufuna kupereka nsembe zawo. Kenako nthawi yoti mupereke mbuzi yanu kwa ansembe yafika. Nthawi yomweyo mukukumbukira kuti munasemphana maganizo ndi m’bale wanu, yemwe n’kuthekanso kuti ali m’khamu la anthuwo kapena mumzinda momwemo. Yesu anafotokoza zimene muyenera kuchita. (Werengani Mateyu 5:24.) Kodi inuyo komanso m’bale wanuyo muyenera kuchita chiyani kuti mukhazikitse mtendere mogwirizana ndi malangizo a Yesuwa? Chongani yankho lolondola m’bokosi lililonse m’munsimu.
ZIMENE MUNGACHITE
-
Kukambirana ndi m’bale wanuyo pokhapokha ngati mukuona kuti palidi chifukwa chomveka chimene anakhumudwira
-
Kumuthandiza kuti aone kuti siinali nkhani yaikulu kapenanso kumufotokozera kuti nayenso analakwitsa
-
Kumumvetsera mwachidwi pamene akufotokoza maganizo ake ndipo ngakhale mukuona kuti inuyo simunalakwe, mungapepese kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha mmene akumvera komanso chifukwa cha zotsatirapo za zimene zinachitikazo
ZIMENE M’BALE WANUYO ANGACHITE
-
Kufotokozera anthu ena mumpingo zimene munamulakwira kuti amuthandize
-
Kukukwiyirani, kumakukumbutsani chilichonse chimene munalakwitsa komanso kumakukakamizani kuti muvomereze kulakwa kwanu
-
Kuzindikira kudzichepetsa ndi kulimba mtima komwe mwasonyeza poyesetsa kuti mukambirane naye ndipo kenako kukukhululukirani ndi mtima wonse
Ngakhale kuti masiku ano sitipereka nsembe zanyama polambira, kodi zimene Yesu anaphunzitsa pa nkhani yokhala mwamtendere ndi abale athu zikugwirizana bwanji ndi kulambira Mulungu?