MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Sankhani Kutumikira Yehova
Ngati ndinu wachinyamata ndipo simunabatizidwe kapena ngati mukuphunzira Baibulo, kodi muli ndi cholinga chofuna kubatizidwa? N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi cholinga choti mubatizidwe? Munthu akadzipereka komanso kubatizidwa amakhala pa ubwenzi wapadera ndi Yehova (Sl 91:1) Amakhalanso ndi mwayi wodzapulumuka. (1Pe 3:21) Ndiye kodi mungatani kuti mudzipereke komanso kufika pobatizidwa?
Muyenera kutsimikizira kuti chimene mukuphunzira ndi choonadi. Mukakhala ndi mafunso muzifufuza kuti mupeze mayankho. (Aro 12:2) Muziganizira mbali zimene mukufunika kusintha, ndipo muzisintha chifukwa chofuna kukondweretsa Yehova. (Miy 27:11; Aef 4:23, 24) Nthawi zonse muzipemphera kwa iye kuti azikuthandizani. Musamakayikire kuti Yehova adzakuthandizani ndi mzimu wake woyera, womwe ndi wamphamvu. (1Pe 5:10, 11) Musamaganize kuti n’kungotaya nthawi kuchita khama kuti muyenerere kubatizidwa. Kutumikira Yehova ndi chinthu chabwino kwambiri kuposa chilichonse.—Sl 16:11.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, ZIMENE MUNTHU ANGACHITE KUTI ABATIZIDWE NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi anthu ena anafunika kulimbana ndi mavuto ati kuti abatizidwe?
-
Kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro chomwe chingakuthandizeni kuti mudzipereke kwa Yehova?
-
Kodi n’chiyani chinachititsa ena kuti achite zinthu zomwe zinawathandiza kuti ayenerere kubatizidwa?
-
Kodi anthu amene amasankha kutumikira Yehova amapeza madalitso otani?
-
Kodi kudzipereka komanso kubatizidwa zimatanthauza chiyani?