February 15-21
NUMERI 3–4
Nyimbo Na. 99 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Utumiki wa Alevi”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Nu 4:15—Tchulani njira imodzi imene tingasonyezere kuti timaopa Mulungu. (w06 8/1 23 ¶13)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Nu 4:34-49 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 2)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Mugawireni chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 15)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) fg phunziro 12 ¶8 (th phunziro 13)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Lipoti la Chaka Chautumiki: (15 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Pambuyo powerenga chilengezo chochokera ku ofesi ya nthambi chokhudza lipoti la chaka chautumiki, funsani ofalitsa omwe munawasankhiratu kuti afotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo mu utumiki chaka chathachi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 121
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 73 ndi Pemphero