CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Utumiki wa Alevi
Yehova anatenga Alevi m’malo mwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli (Nu 3:11-13; it-2 683 ¶3)
Alevi anali ndi mwayi wochita utumiki wapadera kwambiri (Nu 3:25, 26, 31, 36, 37; it-2 241)
Alevi ankagwira ntchito zawo zonse akakhala ndi zaka zapakati pa 30 ndi 50 (Nu 4:46-48; it-2 241)
Alevi aamuna a m’banja la Aroni ankagwira ntchito zaunsembe. Alevi ena onse aamuna ankangowathandiza. N’chimodzimodzinso mumpingo wa Chikhristu masiku ano. Abale ena audindo amasamalira maudindo akuluakulu, pamene ena amagwira ntchito zina ndi zina.