MOYO WATHU WACHIKHRISTU
N’zotheka Kulalikira kwa Aliyense
Mofanana ndi mmene Yehova ankathandizira Aisiraeli, masiku anonso iye akuthandiza anthu ake kuti azichita chifuniro chake. Padziko lonse maofesi a nthambi, madera, mipingo komanso magulu a utumiki amagwira ntchito mogwirizana kuti uthenga wabwino uzilalikidwa. Timalalikira kwa aliyense ngakhalenso anthu achilankhulo china.—Chv 14:6, 7.
Kodi munaganizirapo zophunzira chilankhulo china kuti muthandize munthu wina kuphunzira choonadi? Ngati mulibe nthawi yokwanira kuphunzira chilankhulo china, mukhoza kugwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Language kuti mungophunzira ulaliki wachidule. Mukatero mukhoza kusangalala ngati mmene abale a m’nthawi ya atumwi anasangalalira anthu a m’madera ena atamva “zinthu zazikulu za Mulungu” m’chilankhulo chawo.—Mac 2:7-11.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, KHALANI BWENZI LA YEHOVA—MUZILALIKIRA ANTHU OLANKHULA CHINENERO CHA DZIKO LINA NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi ndi pa nthawi iti pamene mungagwiritse ntchito pulogalamu ya JW Language?
-
Tchulani zinthu zina zimene pulogalamuyi ili nazo.
-
Kodi anthu a m’gawo lanu amalankhula zilankhulo ziti?
-
Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwakumana ndi munthu wachidwi amene amalankhula chilankhulo china?—od 101 ¶39-41.