CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Yehova Amachita Zinthu Mwadongosolo Ndi Anthu Ake
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Numeri.]
Aisiraeli ankamanga mahema m’magulu a mafuko atatuatatu (Nu 1:52, 53; w94 12/1 9 ¶4)
Mumsasa wa Aisiraeli muyenera kuti munali anthu 3 miliyoni kapena kuposa (Nu 2:32, 33; it-1 397 ¶4)
Yehova amafuna kuti anthu ake azimulambira mwadongosolo. Aisiraeli ankalambira Yehova mwadongosolo, ndipo umu ndi mmenenso zilili ndi ife masiku ano.—1Ak 14:33, 40.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimagwirizana ndi mtima wonse ndi zimene gulu la Yehova limachita?’