MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tetezani Banja Lanu
Yehova amaona kuti malumbiro a ukwati ndi nkhani yaikulu. Iye ananena kuti mwamuna ndi mkazi wake sayenera kusiyana. (Mt 19:5, 6) M’gulu la Yehova muli mabanja ambiri osangalala. Komabe, palibe banja limene silikumana ndi mavuto. Tisamakhale ndi maganizo amene anthu ambiri ali nawo oti ngati m’banja muli mavuto, njira yabwino ndi kupatukana kapena kulithetsa. Ndiye kodi Akhristu angateteze bwanji banja lawo?
Mfundo 5 zotsatirazi zingathandize kwambiri.
-
Muziteteza mtima wanu popewa zinthu monga kukopana komanso zosangalatsa zosayenera chifukwa zimenezi zingawononge banja lanu.—Mt 5:28; 2Pe 2:14.
-
Muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu ndipo muziyesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa m’banja lanu.—Sl 97:10.
-
Pitirizani kuvala umunthu watsopano ndipo muzimuchitira mnzanuyo zinthu zing’onozing’ono zosonyeza kukoma mtima. Zimenezi zingachititse kuti azisangalala.—Akl 3:8-10, 12-14.
-
Muzilankhulana mwaulemu komanso mochokera pansi pa mtima.—Akl 4:6.
-
Muzipereka mangawa a m’banja kwa mnzanuyo mwachikondi.—1Ak 7:3, 4; 10:24.
Akhristu akamalemekeza banja, amakhala kuti akulemekezanso Yehova, yemwe analiyambitsa.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, TIYENERA ‘KUTHAMANGA MOPIRIRA’—MUZITSATIRA MALAMULO A MPIKISANO NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Ndi mavuto ati amene banja lingakumane nawo ngakhale kuti linayamba bwinobwino?
-
Kodi mfundo za m’Baibulo zingathandize bwanji anthu amene akuona kuti m’banja mwawo mulibe chikondi?
-
Kodi Yehova anakhazikitsa malamulo ati okhudza banja?
-
Kuti banja liziyenda bwino, kodi mwamuna komanso mkazi ayenera kumachita chiyani?