MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Makolo Muzithandiza Ana Anu Kukhala Odziwa Zinthu
Tikukhala m’dziko limene anthu ambiri amaona kuti zabwino n’zoipa ndipo zoipa n’zabwino. (Yes 5:20) N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amachita zinthu zimene Yehova amadana nazo, monga khalidwe lachiwerewere ndi amuna kapena akazi anzawo. Ana athu akhoza kupusitsidwa ndi anzawo a kusukulu kapena anthu ena kuti achite zoipa. Ndiye kodi mungathandize bwanji ana anu kukonzekera kuti akadzakumana ndi mayesero amenewa kapenanso ena, asadzagonje?
Muzithandiza ana anu kuti azidziwa mfundo za Yehova. (Le 18:3) Mogwirizana ndi msinkhu wawo, muziwaphunzitsa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana. (De 6:7) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndinaphunzitsa ana anga zokhudza kusonyezana chikondi koyenera, kuvala mwaulemu komanso zoti pali zinthu zawo zina zimene ena sayenera kuona? Kodi ana anga angadziwe zoyenera kuchita ngati munthu wina atawaonetsa zinthu zolaula kapena atawauza kuti achite zimene Yehova amadana nazo?’ Kudziwa zoyenera kuchita kungawathandize kuti apewe mavuto ambiri. (Miy 27:12; Mla 7:12) Mukamaphunzitsa ana anu, mumasonyeza kuti mumakonda ana anuwo omwe ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anakupatsani.—Sl 127:3.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, MANGANI NYUMBA YOLIMBA—MUZITETEZA ANA ANU KU “ZINTHU ZOIPA” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
N’chifukwa chiyani makolo ena amavutika kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana?
-
N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuphunzitsa ana awo ‘malangizo ndi kaganizidwe ka Yehova’?—Aef 6:4
-
Kodi gulu la Yehova latipatsa zinthu ziti zomwe zingathandize makolo kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana?—w19.05 12, bokosi
-
N’chifukwa chiyani nthawi zonse muyenera kumalankhula ndi ana anu nkhani zokhudza kugonana, asanakumane ndi mavuto?