Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Misonkhano Yachigawo Imatipatsa Mwayi Wosonyezana Chikondi

Misonkhano Yachigawo Imatipatsa Mwayi Wosonyezana Chikondi

N’chifukwa chiyani timasangalala kwambiri ndi misonkhano yachigawo? Mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Aisiraeli, pamisonkhanoyi timakhala ndi mwayi wolambira Yehova limodzi ndi Akhristu anzathu ambirimbiri. Timaphunzira mfundo zambiri zimene zimatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Timakhalanso ndi mwayi wocheza ndi achibale komanso anzathu. Chifukwa choti timaona kuti misonkhanoyi ndi yofunika kwambiri, timayesetsa kupezekapo masiku onse atatu.

Tikakhala ndi msonkhano, tisamangoganizira mmene ungatithandizire ifeyo. Koma tiziganiziranso mmene tingasonyezere chikondi kwa anzathu. (Aga 6:10; Ahe 10:​24, 25) Timasonyeza kuti sitimangoganizira zofuna zathu zokha, tikamachita zinthu monga kutsegulira ena chitseko kapena kupewa kusunga malo omwe sitiwagwiritsa ntchito. (Afi 2:​3, 4) Pamisonkhano yachigawo timakhala ndi mwayi wopeza anzathu atsopano. Tingachite bwino kukhala ndi cholinga choti msonkhano usanayambe, pa nthawi yopuma kapena ukatha, tidziwane ndi munthu wina. (2Ak 6:13) Anthu amene tingadziwane nawo pa nthawiyi, akhoza kukhala anzathu mpaka kalekale. Chinanso n’chakuti anthu akaona kuti timakondana kwambiri, nawonso angayambe kutumikira Yehova.​​​—Yoh 13:35.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, MSONKHANO WAMAYIKO WAKUTI “CHIKONDI SICHITHA” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi abale ndi alongo amene anapita kumisonkhano ya mayiko ya 2019 anasonyezedwa bwanji chikondi?

  • N’chifukwa chiyani mgwirizano komanso chikondi chimene anthu a Mulungu amasonyezana zili zapadera?

  • Kodi abale a m’Bungwe Lolamulira anasonyeza bwanji chikondi?

  • Kodi inuyo mungachite zinthu ziti pothandiza kuti chikondi chimene timasonyezana pamisonkhano yachigawo chipitirire?

    Kodi chikondi chinathandiza bwanji abale a ku Germany ndi ku South Korea kuti akhale ogwirizana?

  • Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?