MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Achinyamata, Muzicheza Momasuka ndi Makolo Anu
N’chifukwa chiyani muyenera kufotokozera makolo anu momasuka zamumtima mwanu? (Miy 23:26) Chifukwa Yehova anawapatsa udindo wokusamalirani komanso wokuyang’anirani. (Sl 127:3, 4) Zikhoza kukhala zowavuta kuti akuthandizeni ngati mungamawabisire zimene mukuganiza kapena zimene zikukudetsani nkhawa. Komanso simungaphunzire chilichonse pa zimene iwo akumana nazo pa moyo wawo. Kodi n’kulakwa kusauza anthu ena zimene ukuganiza? Sikulakwa. Koma kungakhale kulakwa ngati ukuwapusitsa.—Miy 3:32.
Kodi mungatani kuti muzilankhulana bwino ndi makolo anu? Muzipeza nthawi yabwino kwa inu komanso kwa iwowo. Ngati zingakuvuteni kulankhula nawo, mukhoza kuwalembera kalata yowafotokozera mmene mukumvera. Koma nanga bwanji ngati akufuna kulankhula nanu pankhani imene inuyo simukufuna kukambirana ndi wina aliyense? Muzikumbukira kuti cholinga chawo ndi kukuthandizani. Muziona makolo anu kuti ndi anzanu, osati adani anu. Mukamayesetsa kulankhula ndi makolo anu momasuka, zinthu zidzakuyenderani bwino kwa moyo wanu wonse, ndipo mudzapeza moyo wosatha.—Miy 4:10-12.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MOYO WANGA WACHINYAMATA—KODI NDINGATANI KUTI NDIZILANKHULANA BWINO NDI MAKOLO ANGA? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi Esther ndi Partik anazindikira zotani zokhudza mmene amachitira zinthu pa moyo wawo?
-
Kodi mungaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yesu?
-
Kodi makolo anu akhala akusonyeza bwanji kuti amakukondani?
-
Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzilankhulana ndi makolo anu?