CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzisonyeza Chikondi Chokhulupirika
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Rute.]
Naomi anauza Olipa ndi Rute kuti abwerere ku Mowabu (Ru 1:8-13; w16.02 14 ¶5)
Rute anakana kusiya Naomi komanso Yehova (Ru 1:16, 17; w16.02 14 ¶6)
Timasonyeza ena chikondi chokhulupirika ngati tili odzipereka, okhulupirika komanso ngati tili nawo pa ubwenzi wabwino. Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake okhulupirika. (Sl 63:3) Ifenso tizisonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu ena.—Miy 21:21.