January 3-9
OWERUZA 15-16
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kupereka Mnzako kwa Mdani N’koipa Kwambiri”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Owe 16:1-3—Kodi mavesiwa akutanthauza chiyani? (w05 3/15 27 ¶6)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Owe 16:18-31 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Ulendo Woyamba: Mulungu Amatisamalira—Mt 10:29-31. Muziimitsa vidiyoyi nthawi iliyonse imene pali chizindikiro chosonyeza kuti muime n’kufunsa omvera mafunso omwe ali muvidiyoyi.
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (5 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako mugawireni kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, ndipo yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (th phunziro 9)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Baibulo Linapulumutsa Banja Lathu: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zinathandiza banja lililonse? Kodi kuyambiranso kuchita zinthu zauzimu mokhazikika kunawathandiza bwanji? N’chifukwa chiyani mabanja sakuyenera kusiya kuthana ndi mavuto amene amakumana nawo m’banja mwawo? Kodi mabanja angapeze kuti malangizo auzimu omwe angawathandize?—Yak 5:14, 15.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs mutu 10 ndime 1-12
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 132 ndi Pemphero