KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI
Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Azipezeka Pamisonkhano
Misonkhano yampingo ndi mbali yofunika kwambiri pakulambira koona. (Sl 22:22) Anthu onse amene amasonkhana kuti alambire Yehova, amasangalala komanso amadalitsidwa. (Sl 65:4) Nthawi zambiri ophunzira Baibulo amapita patsogolo mwamsanga ngati akufika pamisonkhano mokhazikika.
Kodi mungathandize bwanji anthu amene mukuphunzira nawo Baibulo kuti azipezeka pamisonkhano? Muziwaitanira kumisonkhano nthawi zonse. Muziwaonetsa vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? Muziwafotokozera kufunika kwa misonkhano. (lff phunziro 10) Mukhoza kuwafotokozera mfundo inayake imene mwaphunzira pamisonkhano kapena zimene mudzaphunzire pamisonkhano yotsatira. Muziwapatsa zinthu zimene zikagwiritsidwe ntchito kumisonkhano. Komanso muziwathandiza, mwina pa nkhani ya mayendedwe. Mukamayesetsa kuitanira ophunzira anu kumisonkhano, mudzasangalala kwambiri akadzayamba kupezekapo.—1Ak 14:24, 25.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI AZIPEZEKA PAMISONKHANO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi Anita anagwiritsa ntchito mwayi uti kuti aitanire Jane kumisonkhano ya mpingo?
-
N’chifukwa chiyani timasangalala kwambiri wophunzira Baibulo akafika pamisonkhano?
-
Kodi Jane anamva bwanji atafika kumisonkhano koyamba?