Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzidziwa Mmene Yehova Amaganizira

Muzidziwa Mmene Yehova Amaganizira

Timafuna kusangalatsa Yehova mu zonse zimene timachita. (Miy 27:11) Kuti tichite zimenezi timayenera kusankha zinthu m’njira imene imasonyeza mmene iye amaganizira ngakhale pamene palibe lamulo lachindunji loti lititsogolere. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi?

Muziphunzira Baibulo nthawi zonse. Nthawi iliyonse imene tikuwerenga Baibulo, timakhala ngati tikucheza ndi Yehova. Tingaphunzire mmene Yehova amaganizira, tikamaona mmene ankachitira zinthu ndi anthu ake komanso tikamaona zitsanzo za anthu amene iye ankaona kuti ankachita zabwino kapena zoipa. Tikafuna kusankha zochita, mzimu woyera ungatithandize kukumbukira zinthu zofunika komanso mfundo zimene tinaphunzira m’Mawu a Mulungu.​—Yoh 14:26.

Muzifufuza. Mukafuna kusankha zochita pa nkhani inayake muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndi mavesi ati kapena nkhani za m’Baibulo ziti zimene zingandithandize kumvetsa bwino mmene Yehova amaonera nkhaniyi?’ Muzipemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni, muzifufuza m’mabuku athu pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira zimene zilipo m’chilankhulo chanu komanso muzigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo zimene zikugwirizana ndi vuto lanulo.​—Sl 25:4.

ONERANI VIDIYO YAKUTI TIYENERA ‘KUTHAMANGA MOPIRIRA’​—MUZIDYA CHAKUDYA CHOPATSA THANZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi mlongo amene ali muvidiyoyi ankakakamizidwa kuchita chiyani?

  • Mutakumana ndi zofanana ndi zimenezi, kodi mungagwiritse ntchito bwanji zinthu zofufuzira?

  • Kodi kupeza nthawi yofufuza komanso kuphunzira Baibulo patokha kumatithandiza bwanji kusankha zinthu mwanzeru?​—Ahe 5:13, 14