Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikonzekereratu Panopa Zimene Mudzachite Mukadzadwala

Muzikonzekereratu Panopa Zimene Mudzachite Mukadzadwala

N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera? Munthu akhoza kudwala kapena kugonekedwa m’chipatala nthawi iliyonse komanso mosayembekezereka. Choncho ndi bwino kukonzekeratu musanadwale n’cholinga choti mudzalandire thandizo labwino. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timalemekeza moyo komanso lamulo la Yehova lokhudza magazi.​—Mac 15:28, 29.

Kodi mungakonzekere bwanji?

  • Mosamala komanso pambuyo popemphera, lembani Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA). a Ofalitsa obatizidwa angatenge khadi lawo kwa mtumiki wa mabuku kapena Khadi la Mwana ngati ali ndi ana aang’ono

  • Ngati ndinu woyembekezera, mungapemphe akulu a mumpingo mwanu kuti akupatseni fomu ya Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-401). Fomuyi ingakuthandizeni kuti musankhe bwino thandizo la chipatala ngati pangakhale mavuto pa nthawi imene muli woyembekezera kapena pa nthawi yochira

  • Ngati mukuyembekezera kulandira thandizo la chipatala lomwe lingadzafune magazi kapena ngati mukuyembekezera kugonekedwa m’chipatala, mungachite bwino kudziwitsiratu akulu padakali nthawi komanso mungadziwitse achipatalawo kuti mukuyembekezera kulandira alendo a Mboni za Yehova

Kodi akulu angathandize bwanji? Iwo angakuthandizeni kudziwa mmene mungalembere khadi la DPA. Komabe, akulu sangakusankhireni thandizo la chipatala kapena kukuuzani maganizo awo pa zinthu zomwe ndi udindo wa aliyense kusankha. (Aro 14:12; Aga 6:5) Mukadziwitsa akulu amumpingo mwanu kuti mukufunika thandizo la chipatala lomwe lingakhudze magazi, iwo adzadziwitsa mwamsanga abale a mu Komiti Yolankhulana ndi Achipatala (HLC).

Kodi a HLC angathandize bwanji? Abale amene amatumikira m’makomiti a HLC anaphunzitsidwa bwino kuti azithandiza madokotala komanso anthu a zamalamulo kumvetsa mmene chipembedzo chathu chimaonera nkhani ya magazi. Iwo angakambirane ndi madokotala za thandizo lachipatala lomwe angakupatseni limene lingaphatikizepo kupewa kukuikani magazi. Ngati pangafunike, iwo angakuthandizeni kupeza dokotala yemwe ndi wosavuta pa nkhani ya magazi.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUNGASANKHE BWANJI ZOYENERA KUCHITA PA NKHANI YA THANDIZO LACHIPATALA LOKHUDZA MAGAZI? KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

  • Kodi mwaphunzira chiyani muvidiyoyi chomwe chingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita ngati mungafunike thandizo lachipatala lomwe likukhudza magazi?

a Phunziro 39 la m’buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale lingakuthandizeni kusankha bwino thandizo lachipatala lokhudza magazi.