CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Musamaiwale Kuti Muli mu Nthawi Yamapeto
Yehova anachenjeza Ayuda kuti adzawakana akapitiriza kuchita zoipa (2Mf 24:2, 3; w01 2/15 12 ¶2)
Yehova anagwiritsa ntchito Ababulo kuti awononge Yerusalemu mu 607 B.C.E. (2Mf 25:8-10; w07 3/15 11 ¶10)
Yehova anapulumutsa anthu amene anamvera machenjezo ake (2Mf 25:11)
Kwa zaka zambiri, Yehova wakhala akuchenjeza anthu padziko lapansi kuti adzawononga “anthu osaopa Mulungu.”—2Pe 3:7.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndimagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene ndapeza kuti ndithandize ena kudziwa zimene Mulungu akutichenjeza?’—2Ti 4:2.