February 12-18
SALIMO 5-7
Nyimbo Na. 118 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzikhalabe Okhulupirika Posatengera Zimene Ena Akuchita
(10 min.)
Nthawi zina, Davide ankakhumudwa chifukwa cha zochita za anthu ena (Sl 6:6, 7)
Iye anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize (Sl 6:2, 9; w21.03 15 ¶7-8)
Davide anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova chifukwa ankamudalira kwambiri (Sl 6:10)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndikuyesetsa kulimbitsa chikhulupiriro changa kuti ndizikhalabe wokhulupirika kwa Yehova posatengera zimene ena akuchita?’—w20.07 8-9 ¶3-4.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Sl 5:9—Kodi mmero wa anthu oipa ukufanana bwanji ndi manda otseguka? (it-1 995)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 7:1-11 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 1 mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Popanda kutchula mfundo ya m’Baibulo, pezani njira yomwe ingathandize munthu amene mukukambirana naye kudziwa kuti ndinu wa Mboni za Yehova. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba akufuna kukangana nanu. (lmd phunziro 4 mfundo 5)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(4 min.) Chitsanzo. ijwfq 64—Mutu: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lawo? (lmd phunziro 3 mfundo 4)
Nyimbo Na. 99
8. Lipoti la Chaka cha Utumiki
(15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo powerenga chilengezo chochokera ku ofesi ya nthambi chokhudza lipoti la chaka cha utumiki, funsani omvera kuti afotokoze zinthu zabwino zomwe zili mu Lipoti la Chaka cha Utumiki cha 2023 la Mboni za Yehova Padziko Lonse. Funsani ofalitsa omwe munawasankhiratu kuti afotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo mu utumiki chaka chathachi.
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 5 ¶16-22, bokosi patsamba 42