Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

February 19-25

SALIMO 8-10

February 19-25

Nyimbo Na. 2 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Ndidzakutamandani Inu Yehova”

(10 min.)

Yehova amatichitira zinthu zabwino kwambiri (Sl 8:3-6; w21.08 3 ¶6)

Timatamanda Yehova pouza ena zokhudza ntchito zake zodabwitsa (Sl 9:1; w20.05 23 ¶10)

Timamutamandanso tikamamuimbira nyimbo ndi mtima wonse (Sl 9:2; w22.04 7 ¶13)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingatamande Yehova m’njira zinanso ziti?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 8:3—Kodi wolemba masalimo ankatanthauza chiyani pamene anatchula zala za Mulungu? (it-1 832)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba wakuuzani kuti sakhulupirira Mulungu. (lmd phunziro 5 mfundo 4)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pa ulendo wapita, munthuyo anakuuzani kuti sakhulupirira Mulungu, komabe akhoza kulola kuti mumusonyeze umboni wotsimikizira kuti kuli Mlengi. (th phunziro 7)

6. Nkhani

(5 min.) w21.06 6-7 ¶15-18—Mutu: Muzithandiza Wophunzira Baibulo Wanu Kuti Azitamanda Yehova. (th phunziro 10)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 10

7. Kodi Tingalalikire Bwanji Mwamwayi M’njira Yosavuta?

(10 min.) Nkhani yokambirana.

Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timatamanda Yehova ndi kulalikira kwa anthu amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. (Sl 35:28) Poyamba, tikhoza kumachita mantha kuti tilalikire munthu mwamwayi. Komabe, ngati titaphunzira mmene tingayambire kukambirana ndi munthu komanso mmene tingapitirizire kukambirana naye m’njira yosavuta, tikhoza kukhala aluso n’kumasangalala kugwiritsa ntchito njira imeneyi ya ulaliki.

Onerani VIDIYO yakuti Muzikhala Okonzeka Kulalikira “Uthenga Wabwino Wamtendere”—Muziyamba Ndinu Kuwalankhula. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi mwaphunzira chiyani muvidiyoyi chomwe chingakuthandizeni kukhala aluso polalikira mwamwayi?

Onani mfundo zotsatirazi zomwe zingakuthandizeni:

  •   Mukamachoka kunyumba kwanu, muzioneratu mwayi umene mungakhale nawo woti muyambe kukambirana ndi anthu. Muzipemphera, kumupempha Yehova kuti akuthandizeni kukumana ndi anthu a mtima wabwino

  •   Muzikhala aubwenzi ndipo muzisonyeza chidwi kwa anthu amene mwakumana nawo. Muziyesetsa kudziwa zinthu zina zokhudza munthu amene mukukambirana nayeyo, zomwe zingakuthandizeni kudziwa mfundo ya m’Baibulo imene ingamufike pamtima

  •   Ngati n’zotheka, mungauzane kumene mumakhala kapena kupatsana manambala a foni

  •   Musamakhumudwe ngati mungasiye kulankhulana musanafike pomulalikira

  •   Muzimuganizirabe pambuyo pokambirana naye. Muzipitiriza kumusonyeza chidwi pomutumizira linki ya vesi linalake kapena ya nkhani ya pa jw.org

Yesani izi: Ngati munthu wina atakufunsani kuti, ‘Kodi zakuyenderani bwanji Loweruka ndi Lamlungu lapitali?,’ mungamuuze zimene mwaphunzira kumisonkhano kapena ntchito imene mumagwira yophunzitsa anthu Baibulo.

8. Zofunika Pampingo

(5 min.)

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 65 ndi Pemphero