Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

January 15-21

YOBU 36-37

January 15-21

Nyimbo Na. 147 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhulupirira Lonjezo la Mulungu Loti Adzatipatsa Moyo Wosatha?

(10 min.)

Yehova adzakhalapo mpaka kalekale (Yob 36:26; w15 10/1 12 ¶4-13 ¶1)

Yehova ali ndi nzeru komanso mphamvu zochititsa moyo kuti usafe (Yob 36:27, 28; w20.05 22 ¶6)

Iye amatiphunzitsa zomwe tingachite kuti tidzapeze moyo wosatha (Yob 36:4, 22; Yoh 17:3)


Tikamakhulupirira lonjezo la Mulungu loti adzatipatsa moyo wosatha, timatha kupirira mavuto osiyanasiyana amene timakumana nawo.—Ahe 6:19; w22.10 28 ¶16.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Yob 37:20—Kodi anthu ankadziwitsana bwanji mauthenga m’mayiko akale omwe anatchulidwa m’Baibulo? (it-1 492)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 3 mfundo 3)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 2 mfundo 5)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Nkhani. ijwfq 57 ¶5-15—Mutu: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Ankazunzidwa pa Nthawi ya Ulamuliro wa Nazi? (th phunziro 18)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 49

7. Muzikonzekereratu Zimene Mudzachite Mukadzadwala Kapena Mukadzafunika Kuchitidwa Opaleshoni

(15 min.) Nkhani yokambirana. Ikambidwe ndi mkulu.

Gulu la Yehova linatipatsa zinthu zotithandiza kumvera lamulo la Mulungu lokhudza magazi. (Mac 15:28, 29) Kodi zinthu zimenezi mumazigwiritsa ntchito moyenera?

Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA) ndi Khadi la Mwana (ic): Makadi amenewa amafotokoza zimene munthu anasankha pa nkhani yokhudza magazi. Ofalitsa obatizidwa akhoza kupempha khadi la DPA kapena Khadi la Mwana ngati ali ndi ana kwa mtumiki wa mabuku. Makadiwa muziyenda nawo nthawi zonse. Ngati mukufunika kusaina kapena kusintha zinthu zina pa khadi lanu, musazengereze.

Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-401) ndi Mfundo Zofunika Kukumbukira Tikafunika Thandizo la Opaleshoni Kapena la Matenda a Khansa (S-407): Mafomuwa amatithandiza kuti tikhale okonzeka bwino pa nkhani ya thandizo lachipatala lomwe tingalandire komanso pa nkhani ya magazi. Ngati ndinu oyembekezera kapena mukufunika kuchitidwa opaleshoni kapenanso kulandira thandizo la matenda a khansa, pemphani akulu kuti akupatseni fomu yoyenerera.

Komiti Yolankhulana ndi Achipatala (HLC): Abale a HLC anaphunzitsidwa bwino za mmene angathandizire madokotala komanso ofalitsa pa nkhani yokhudza magazi. Akhoza kukambirana ndi dokotala amene akukuthandizani za njira zina zimene angagwiritse ntchito m’malo mokuikani magazi. Ngati pangafunikire, angakuthandizeni kupeza dokotala amene angalemekeze zosankha zanu. Iwo amapezeka tsiku lililonse, nthawi iliyonse kwa maola onse 24. Muzidziwitsa a HLC mwamsanga ngati mwagonekedwa m’chipatala, mukufunika kuchitidwa opaleshoni kapena ngati mukufunika kulandira thandizo la matenda a khansa, ngakhale zitaoneka kuti sizikhudzana ndi magazi. Ngati ndinu oyembekezera mukufunikanso kuchita zimenezi. Ngati mukufunikira thandizo, mungapemphe akulu kuti akupatseni manambala a abale a HLC.

Onerani VIDIYO yakuti Kodi Makomiti Olankhulana ndi Achipatala Amathandiza Bwanji? Kenako funsani mafunso awa:

Kodi a HLC angakuthandizeni bwanji ngati mukufunika thandizo lachipatala kapena kuchitidwa opaleshoni?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 67 ndi Pemphero