Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

January 22-28

YOBU 38-39

January 22-28

Nyimbo Na. 11 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kodi Mumapeza Nthawi Yoona Chilengedwe?

(10 min.)

Atalenga dzikoli, Yehova anapeza nthawi yoti aone zomwe analengazo (Ge 1:10, 12; Yob 38:5, 6; w21.08 10 ¶7)

Angelo anapeza nthawi yoti aone chilengedwe cha Yehova (Yob 38:7; w20.08 14 ¶2)

Tingamadalire kwambiri Yehova ngati timapeza nthawi yoona ndi kuyamikira zimene iye analenga (Yob 38:32-35; w23.03 17 ¶8)

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Yob 38:8-10—Kodi mavesiwa akutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova monga Wopereka Malamulo? (it-2 222)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Sonyezani mmene mwaulemu mungasiyire kukambirana ndi munthu amene akuoneka kuti sakufuna kulankhula nanu. (lmd phunziro 2 mfundo 3)

5. Ulendo Wobwereza

(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pa ulendo wapita, mwininyumbayo anakuuzani kuti wachibale wake kapena mnzake wamwalira. (lmd phunziro 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 1—Mutu: Zinthu Zomwe Zikuchitika Masiku Ano Zikusonyeza Kuti Posachedwapa Zinthu Zisintha. (th phunziro 16)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 111

7. Kuchita Chidwi ndi Chilengedwe Kumatithandiza Kuti Tiziganizira Zinthu Zofunika Kwambiri

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Pa nthawi imene Yobu ankatsutsidwa ndi anzake atatu komanso Satana, iye ankangoganizira za mavuto ake komanso zinthu zopanda chilungamo zomwe zinkamuchitikira.

Werengani Yobu 37:14. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi Yobu ankafunika kuchita chiyani kuti ayambenso kuona zinthu moyenera?

Tikapanikizika ndi mavuto, kuchita chidwi ndi chilengedwe kungatithandize kuti tizikumbukira kuti Yehova ndi wamkulu, kungatilimbikitse kuti tikhalebe okhulupirira komanso kungatithandize kuti tizimudalira kwambiri kuti atisamalira.—Mt 6:26.

Onerani VIDIYO yakuti Zimene Tikuphunzira M’buku la Yobu—Zimene Zinyama Zimatiphunzitsa. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi vidiyoyi yakulimbikitsani bwanji kuti muzidalira kwambiri Yehova?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 4 ¶13-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 54 ndi Pemphero