Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

January 8-14

YOBU 34-35

January 8-14

Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Moyo Ukamaoneka Kuti Ndi Wokondera

(10 min.)

Tizikumbukira kuti Yehova sachititsa zinthu zopanda chilungamo (Yob 34:10; wp19.1 8 ¶2)

Zingamaoneke ngati anthu amene amachita zoipa salangidwa, komatu iwo sangabisale kwa Yehova (Yob 34:21-26; w17.04 10 ¶5)

Njira yabwino yothandizira anthu amene akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo ndi kuwaphunzitsa zokhudza Yehova (Yob 35:9, 10; Mt 28:19, 20; w21.05 7 ¶19-20)

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Yob 35:7—Kodi Elihu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Kodi [Mulungu] amalandira chiyani kuchokera kwa inu?” (w17.04 29 ¶3)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pemphani mwininyumba kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 10 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Sonyezani munthu amene ali ndi ana mmene angapezere pa jw.org malangizo othandiza makolo kulera ana. (lmd phunziro 1 mfundo 4)

6. Kuphunzitsa Anthu

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 58

7. Kodi Ndinu Wofunitsitsa ‘Kulalikira Mawu’ Mwamwayi?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Lalikira mawu. Uzilalikira modzipereka.” (2Ti 4:2) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “modzipereka,” nthawi zina ankagwiritsidwa ntchito ponena za msilikali kapena mlonda amene nthawi zonse ankakhala wokonzeka. Choncho mawu a palembali akufotokoza bwino kuti nthawi zonse tizikhala tcheru kuti tipeze mpata woyamba kukambirana ndi anthu zokhudza Baibulo pamene tikulankhula nawo.

Kukonda Yehova komanso kuyamikira zonse zimene amatichitira n’zimene zimatithandiza kuti tiziuza ena zokhudza makhalidwe ake abwino.

Werengani Salimo 71:8. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi mumakonda kuuza anthu ena zinthu zabwino ziti zokhudza Yehova?

Kukonda anthu kumatithandizanso kuti tizilalikira mwamwayi.

Onerani VIDIYO yakuti Anthu Ambirimbiri Anapeza Choonadi. Kenako funsani mafunso otsatirawa:

  •   Kodi kulalikira mwamwayi kunathandiza bwanji kuti anthu ambiri aphunzire choonadi cha m’Baibulo?

  •   Kodi kuphunzira choonadi kunawathandiza bwanji anthu amene anasiya tchalitchi chawo?

  • Kodi kukonda anthu kumatithandiza bwanji kuti tizilalikira mwamwayi?

  • N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti kulalikira mwamwayi ndi njira yabwino yothandizira anthu kudziwa Yehova?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 138 ndi Pemphero