Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

February 24–March 2

MIYAMBO 2

February 24–March 2

Nyimbo Na. 35 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuikirapo Mtima Tikamaphunzira Baibulo Patokha?

(10 min.)

Kuti tisonyeze kuti timaona choonadi kukhala chamtengo wapatali (Miy 2:3, 4; w22.08 18 ¶16)

Kuti tizisankha zinthu mwanzeru (Miy 2:5-7; w22.10 19 ¶3-4)

Kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu (Miy 2:11, 12; w16.09 23-24 ¶2-3)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingasinthe zinthu ziti kuti ndiziphunzira Baibulo pandekha mokhazikika?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Miy 2:7—Kodi Yehova amakhala bwanji “chishango kwa anthu amene amachita zinthu mokhulupirika”? (it-1 1211 ¶4)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Musonyezeni mmene angapezere mfundo zothandiza mabanja pa jw.org. (lmd phunziro 1 mfundo 3)

5. Ulendo Wobwereza

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’patseni magazini yomwe ili ndi nkhani imene anachita nayo chidwi pa ulendo wapita. (lmd phunziro 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 8—Mutu: Mwamuna Ndi Mkazi Wake Ayenera Kukhala Okhulupirika. (th phunziro 13)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 96

7. Kodi Mumakonda Kufunafuna Chuma Chobisika?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Achinyamata, kodi mumakonda kufunafuna chuma chobisika? Ngati ndi choncho, Baibulo likukulimbikitsani kuti muyambe kufunafuna chuma chamtengo wapatali kwambiri m’chilengedwe chonse chomwe ndi kudziwa Mulungu. (Miy 2:4, 5) Mungapeze chumachi ngati mumawerenga Baibulo tsiku lililonse komanso ngati mumafufuza kuti mumvetse zomwe mukuwerengazo. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kukhala osangalala komanso mudzadziwa zambiri.

  • Kodi mungadzifunse mafunso ati mukamawerenga Baibulo? (w24.02 32 ¶2-3)

  • Kodi mungagwiritse ntchito zinthu ziti kuti mupeze mayankho?

Mavidiyo akuti Phunzirani kwa Anzake a Yehova angakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muziganizira mozama zimene mukuwerenga m’Baibulo.

Onerani VIDIYO yakuti Phunzirani kwa Anzake a Yehova—Abele.

Werengani Genesis 4:2-4 ndi Aheberi 11:4. Kenako funsani mafunso awa:

  • Kodi Abele anasonyeza bwanji kuti anali mnzake wa Yehova?

  • Kodi anatani kuti azikhulupirira kwambiri Yehova?

  • Kodi mungatani kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 102 ndi Pemphero