Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

February 3-9

MASALIMO 144-146

February 3-9

Nyimbo Na. 145 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Osangalala Ndi Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova”

(10 min.)

Yehova amadalitsa anthu amene amamudalira (Sl 144:11-15; w18.04 32 ¶3-4)

Timasangalala ndi chiyembekezo chathu (Sl 146:5; w22.10 28 ¶16-17)

Anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova adzakhala osangalala mpaka kalekale (Sl 146:10; w18.01 26 ¶19-20)

Tikamatumikira Yehova mokhulupirika, tikhoza kukhala osangalala kwambiri ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 145:15, 16—Kodi mavesiwa akutithandiza bwanji kuona mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi zinyama? (it-1 111 ¶9)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo wakuuzani kuti amaphunzira ku yunivesite. (lmd phunziro 1 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Gwiritsani ntchito vidiyo yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (lmd phunziro 7 mfundo 4)

6. Nkhani

(4 min.) lmd zakumapeto A mfundo 7—Mutu: Mkazi Ayenera ‘Kulemekeza Kwambiri Mwamuna Wake.’ (th phunziro 1)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 59

7. Yehova Amafuna Kuti Tizisangalala

(10 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova ndi Mulungu wachimwemwe. (1Ti 1:11) Anatipatsa mphatso zambiri zabwino zomwe zimasonyeza kuti amatikonda komanso amafuna kuti tizisangalala. (Mla 3:12, 13) Taganizirani mphatso ziwiri izi, chakudya komanso kaphokoso kosangalatsa.

Onerani VIDIYO yakuti Chilengedwe Chimasonyeza Kuti Yehova Amafuna Tizisangalala—Chakudya Chokoma Komanso Kaphokoso Kosangalatsa. Kenako funsani funso ili:

  • Kodi mphatso ya chakudya komanso kaphokoso kosangalatsa zimatitsimikizira bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala?

Werengani Salimo 32:8. Kenako funsani funso ili:

  • Kodi kudziwa kuti Yehova amafuna kuti muzisangalala kumakuthandizani bwanji kuti muzimvera malangizo ake omwe amapereka kudzera m’Baibulo komanso gulu lake?

8. Zofunika Pampingo

(5 min.)

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 22 ¶1-6

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero