Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

January 27–February 2

MASALIMO 140-143

January 27–February 2

Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Mapemphero Anu Opempha Thandizo

(10 min.)

Muzikhala okonzeka kulandira malangizo kapena uphungu (Sl 141:5; w22.02 12 ¶13-14)

Muziganizira zimene Yehova anachita populumutsa anthu ake m’mbuyomu (Sl 143:5; w10 3/15 32 ¶4)

Muziyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera (Sl 143:10; w15 3/15 32 ¶2)

Mu Masalimo 140-143, muli mapemphero a Davide opempha thandizo komanso muli mawu osonyeza kuti iye ankachita zinthu mogwirizana ndi zimene ankapemphazo.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 140:3—N’chifukwa chiyani Davide anayerekezera lilime la anthu oipa ndi lilime la njoka? (it-2 1151)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Sinthani nkhani n’kuyamba kukambirana zokhudza Baibulo pambuyo pothandiza munthuyo m’njira inayake. (lmd phunziro 3 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Munthuyo wakuuzani kuti ali bize. (lmd phunziro 7 mfundo 3)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Chitsanzo. ijwfq 21—Mutu: N’chifukwa Chiyani Mumakana Kuikidwa Magazi? (th phunziro 7)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 141

7. Muzikonzekereratu Zimene Mudzachite Mukadzadwala Kapena Mukadzafunika Kuchitidwa Opaleshoni

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova amalonjeza kuti iye ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.” (Sl 46:1) Zimene zimachitika munthu akadwala kapena akafunika kuchitidwa opaleshoni zimayambitsa nkhawa. Komabe, Yehova anatipatsa zonse zomwe timafunikira pa zochitika ngati zimenezi. Mwachitsanzo, gulu lake linatipatsa khadi lopatsa munthu mphamvu zotiimira pa thandizo lakuchipatala (DPA), Khadi la Mwana, a mafomu ena a zachipatala b kuphatikizapo Makomiti Olankhulana ndi Achipatala (HLC). Zinthu zimenezi zimatithandiza kuti tizimvera lamulo la Mulungu lokhudza magazi.—Mac 15:28, 29.

Onerani VIDIYO yakuti Kodi Mwakonzekera Zimene Mudzachite Mukadzafunikira Thandizo la Chipatala? Kenako funsani mafunso otsatirawa:

  • Kodi kulemba fomu ya DPA kwathandiza bwanji anthu ena?

  • Kodi fomu yakuti Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-401) inathandiza bwanji ena?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuuza a HLC mwamsanga ngati taona kuti tikhoza kugonekedwa m’chipatala, kuchitidwa opaleshoni, kapena kulandira thandizo la matenda monga a khansa ngakhale zitaoneka kuti sizikhudzana ndi magazi?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 21 ¶14-22

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero

a Ofalitsa obatizidwa angatenge khadi lawo la DPA kapena Khadi la Mwana kwa mtumiki wa mabuku.

b Mungapemphe kwa akulu ngati mukufuna fomu ya Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-401), fomu ya Mfundo Zofunika Kukumbukira Tikafunika Thandizo la Opaleshoni Kapena la Matenda a Khansa (S-407), komanso fomu ya Mmene Makolo Angatetezere Ana Awo Kuti Asapatsidwe Magazi (S-55).